Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ntchito Zoweruza Milandu Ziyamba Kuyenda Mwachangu

$
0
0

Ntchito zoweruza milandu mmabwalo osiyanasiyana mdziko muno ati ziyamba kuyenda mwachungu potsatira kusintha kwa zipangizo  zogwilira ntchitoyi zomwe mabwalo aakulu alandira mdziko muno.

Mmodzi mwa akuluakulu oweruza milandu ku bwalo lalikulu la Appeal mu mzinda wa Blantyre Justice Dastain Mwaungulu ndi yemwe wanena izi polankhula ndi  Radio Maria Malawi pomwe wailesiyi imafuna kudziwa zina mwa zifukwa zomwe zimachedwetsa kaweruzidwe ka milandu mmabwalo  a milandu mdziko muno.

Justice Mwaungulu wati pali mavuto ambiri omwe amachititsa kuti anthu azichedwa kulandira chilungamo pankhani zawo monga kusowa kwa zipangizo za makono.

Iwo ati zinthu ziyamba kuyenda bwino pomafika chaka cha mawa, potsatira zipangizo zomwe mabwalowa alandira kuchokera ku boma.

Justice Mwaungulu wati ngakhale mabwalo a milandu mdziko muno akhala akukumana ndi mavuto pa kagwiridwe ka ntchito zake, dziko lino likupitiliza kukhala mgulu la mayiko omwe makhothi awo amaweruza milandu mwachilungamo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>