Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wapereka uthenga opepesa ku mabanja omwe ataya abale awo pangozi yomwe yachitika mdziko la China makina a fakitore ina ataphulika mchigawo chakumpoto kwa dzikolo.
Iye wati ndi wokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya anthu omwe amwalira pangoziyo ndipo wati akhala akupemphelera anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.