Mayi wina wa zaka 50 m’boma la Ntchisiwadzipha podzimangilira ku mtengo kamba koti anapezeka ndi matenda a khansa.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati izi zachitika usiku wa lachiwiri sabata ino m`mudzi mwa Khadani kwa mfumu yayikulu Chikho m’bomalo.
Iwo ati malemuyo wakhala akudwala komanso kugonekedwa mchipatala chachikulu cha Ntchisi kamba ka vuto la matendawa kwa nthawi yaitali.
Malinga ndi Sergent M’bumpha malemuyu wakhala akudwala matendawa kwa nthawi yaitali ndipo wakhala akugonekedwa kangapo konse ku chipatala chachikulu cha Ntchisi.
Mamuna wake wa malemuyo Zamtima Kanjedza atawona kuti sizikusintha ati pa 11 mwezi uno anaganiza zotengera mkazi wawoyo kwa sing’anga wa mmudzi wina wa m’bomalo.
Atafika kwa sing’angayo ati sanathe kulandira thandizo kaamba koti mayiyo anali atafooka kwambiri.
A M’bumpha ati usiku wa lachiwiri sabata ino ndi pamene amazindikira kuti malemuyo sakuoneka, atayang’ana anapeza kuti wamwalira atadzimangilira pa mtengo.
Malipoti achipatala asonyeza kuti malemuyo wamwalira kamba koti amalephera kupuma ndipo kuti palibe yemwe akumuganizira kuti wachita chiwembucho.
Malemuyo Selina Zamtima ankachokera mmudzi mwa Kankowe kwa mfumu yayikulu Nthondo m’boma lomwelo la Ntchisi.