Mtsogoleri wadziko la South Sudan A Salva Kiir wati asayinira mgwirizano odzetsa mtendere pakati pa iye ndi magulu owukira boma mdzikolo.
Pulezidenti Kiir lolemba analonjeza kuti asainira panganoli pakatha sabata ziwiri.
Malipoti a NEWS 24 ati mlembi wa boma la dziko la United States A John Kerry awuza Pulezidenti Kiir kuti zomwe akuchita ndi kulephera utsogoleri posafuna kusayinira panganolo kamba koti nkhondo yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo kuyambira mchaka cha 2013, yapha anthu zikwizikwi.
Pulezidenti Kiir wati akuyenera kuti afunse maganizo koma walonjeza a Kerry kuti asayinira panganolo masiku akudzawa.
Padakali pano mtsogoleri wa kumbali yowukira boma a Rik Marshal mdzikolo wasayinira kale panganolo.