Bungwe la Eye of the Child lati ndi lokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mwana wazaka zisanu yemwe waphedwa masiku apitawa mumzinda wa Lilongwe pofuna kugwiritsa ntchito ziwalo zake ngati zizimba zokulitsira bizinezi.
Bungweli lati mpofunika kuti boma lichitepo kanthu pothana ndi mchitidwe waupandu omwe anthu ena kuphatikizapo madotolo a mankhwala a zitsamba akuchita mdziko muno.
Kudzera mchikalata chomwe bungweli latulutsa lamulungu,mkulu wa bungwe a Maxwell Matewere apempha boma kudzera mmakhonsolo a maboma onse kuti likhazikhazikitse malamulo a padera omwe aziletsa asing’ana kugwira ntchito zawo mdziko muno.
Iwo ati mbiri ya kuphedwa kwa ana komanso alubino, ikhudze m’Malawi aliyense ndipo apempha magulu osiyanasiyana kuti agwirane manja ndi bungweli polimbikitsa boma kudzera kunyumba ya malamulo kuti likhazikitse malamulo kuti liwunikenso malamulo okhudza ufiti pofuna kuteteza magulu osiyanasiyana omwe akuchitiridwa nkhanza zomwe zikukolezeredwa ndi madotolo a mankhwala azitsamba.