Dziko la Egypt linayitanitsa kazembe wa dziko la Britain mdzikolo John Casson, chifukwa chodzudzula bwalo la milandu mdzikolo lomwe lalamula atolankhani atatu a wailesi ya kanema ya Al-Jazeera kuti akakhale kundende kwa zaka zitatu aliyense, litawapeza olakwa pa mulandu ofalitsa nkhani yabodza.
Akuluakulu a boma anayitanitsa kazembeyo iye atanena kuti ndi okhudzidwa kwambiri ndi chigamulo chomwe bwalo la milandulo lapereka kwa atolankhaniwo.
Boma la Egypt lati zomwe kazembeyo walankhula n’kulowera ntchito za makhothi zomwe ndi zosavomerezeka.
Anthu ambiri omwe athilirapo ndemanga pa nkhaniyi kudzera pamakina a intaneti, ati mpofunika kuti dziko la Britain lichotse ntchito kazembeyo.
Polankhula pambuyo pokumana ndi akuluakulu a bomawo, kazembeyo wati zomwe iye walankhula ndi maganizo a dziko la Britain pa mulandu wa atolankhaniwo kamba koti ena mwa atolankhani omwenso akhala akuyimbidwa mulanduwu ndi a ku Britain.