Anthu awiri afa ndipo ena asanu ndi anayi avulala minibus yomwe anakwera itagubuduzika dalaivala wake atalephera kuwongolera m’boma la Zomba.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali a Patricio Supriano watsimikiza za nkhaniyi.
Iwo ati minibus-yo yomwe ndi ya mtundu wa Toyota Hiace nambala yake ndi BS 8345 amayendetsa ndi a Willy Kapinga, ndipo yagubuduzika teyala lake litaphulika zomwe zinachititsa kuti alephere kuwongolera moyenera.
Anthu awiriwo amwalira pa malo pomwepo ndipo asanu ndi anayiwo akulandira thandizo ku chipatala chachikulu cha Zomba.