Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco watumiza uthenga wa chipepeso kwa abale a anthu omwe akhudzidwa ndi mphepo ya mkuntho yomwe yachitika pa doko la Caribean .
Mu uthengawo iye wati ndi okhudzidwa ndi imfa zomwe zadza kamba ka mphepoyo ndipo wati alumikizana ndi ndi mabanja okhudzidwa komanso onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi munjira zosiyanasiyana, kudzera mmapemphero.
Iye walimbikitsa mabanjawa kuti akhale ndi chiyembekezo chabwino komanso akhale mwa mtendere.