Episkopi wa dziko la Swaziland wapempha anthu m’dzikolo kuti akhale ndi mwambo wa mapemphero potsatira ngozi ya pansewu yomwe inapha atsikana pafupifupi makumi asanu omwe adali paulendo okapikisana nawo pamwambo osankha mkazi watsopano wa mfumu Mswati ya dzikolo.
Malipoti a Catholic News Agency ati anthu mdzikoli akuyenera kukhala ndi mapemphero apadera pofuna kupempha chitetezo kwa mulungu kuti dzikoli lipewe ngozi za mtunduwu.
Episkopiyu wapempha anthu mdzikoli kuti akuyenera nthawi zonse kukhala ndi nthawi yopemphera osati kudikira ngozi za mtunduwu kuti zichitike.