Matupi khumi a asilikali a dziko la Uganda omwe anafa, gulu la zauchifwamba la Al-shabab litachita zamtopola kumalo omwe asilikaliwa amakhaka omwe ali pamtunda wamakilomita 90 kumm’wera chakunzambwe kwa mzinda wa Mogadishu apita nawo m`dziko la Uganda.
Malinga ndi malipoti a BBC asilikali khumi ndi awiri a m`dziko la Uganda anaphedwa ndi zigawenga zaAl-shabab lachiwiri ndipo zigawengazo zinapha asilikali okwana 70.
Omwe anaona izi zikuchitika ati zigawengazo zinaphulitsa bomba la timkenawo m`galimoto pachipata cholowera pamalowa ndipo kenako zinayamba kuwombera komwe kunatenga ola limodzi.
Asilikali a dziko la Uganda ali m`gulu la asikali 22 sauzande a bungwe la African Union AU omwe pamodzi ndi asilikali a dziko la Uganda akulimbana ndi zigawengazi.