Mtsogoleri wa dziko la Guatemala a Perezi Molina watula pansi udindo wake komanso amangidwa kamba komuganizira kuti amachita zakatangale.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Pulezidenti Morina watula pansi udindowu potsatira chisankho cha Pulezidenti chomwe chikuyembekezeka kuchitika lamulungu m’dzikolo.
Pulezidentiyu ati amumanga kamba koti akumuganizira kuti amachita zakatangale ndi cholinga choti asamalipire msokho pa katundu yemwe amagula kunja kwa dzikolo.
Pakadali pano Pulezidentiyu akumusunga ku ndende ya asilikali ya Matamoros m`dzikolo ndipo yemwe anali wachiwiri wa Pulezidezidentiyu Mayi Roxana Baldetti anamangidwanso m`mwezi wa May chaka chino atangotula pansi udindo wake.
Anthu a m`dziko la Guatemala achita chisankho cha Pulezidenti lamulungu ndipo yemwe asakhidwe adzayamba kulamulira dzikolo mwezi wa January chaka cha mawa.