Matupi a anthu 61 a mdziko la Indonesia omwe anafa pa ngozi ya bwato lomwe anakwera litamila lachinayi sabata yatha mdziko la Malaysia, apezeka lolemba.
Malinga ndi malipoti a nyuzi 24 anthuwo amalowa mdzikolo mosavomerezeka ndipo ambiri omwe afa pa ngoziyo ndi amuna.
Malipoti ati ngoziyo inachitaka pomwe bwatolo linagubuduzika kamba koti linanyamula anthu ambiri komanso nyengo pa tsikulo sinali bwino.
Dziko la Malaysia likusungira anthu ovomerezeka ndi osavomerezeka mdzikolo ochokera mdziko la Indonesia pafupifupi 6 miliyoni potsatira mwayi wa ntchito.