Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chipani cha SBVM Chikondwelera Zaka 90 Chikhazikitsire

$
0
0

Asisteri a Chipani cha atumiki a maria virgo woyera Sisters of the Blessed Virgin Mary SBVM mu mpingo wakatolika awayamikira kamba ka ntchito zosiyanasiyana zomwe akhala akugwia m’dziko muno.

 

Episkopi wa dayosizi ya Chikwawa olemekezeka Ambuye Peter Musikuwa ndi omwe anena izi pa mwambo wa nsembe ya ukaristia yokondwelera kuti chipanichi chakwanitsa zaka makumi asanu ndi anayi  chikutumikira mulungu ndi mpingowu mdziko muno.

 

Iwo ati mpingo umayamika ntchito zomwe asistere mzipani zosiyanasiyana mu mpingowu amagwira mdziko muno.

 

Ambuye Musikuwa anapitiliza ndi kunena kuti kwa zaka 90 zapitazi, asisitere mu chipanichi awonetsadi kuti ndi atumiki eni eni a mulungu, kamba ka ntchito zomwe akhala akugwira zomwenso zathandiza kukulitsa moyo wauzimu ngakhalenso wa thupi pakati pa akhristu mu mpingo wa Katolika  ndi dziko lino.

 

Chipanichi chinayamba  m'chaka cha 1925 mwa zina chakhala chikugwira ntchito zamaphunziro, zaumoyo ndinso kutumikira m’magawo ena mu mpingo wakatolika m`dziko muno.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>