Nthambi ya bungwe la United Nations lowona za Umoyo la World Health Organisation WHO lati chiwerengero cha imfa za ana osakwana zaka zisanu chatsika ndi mapereseti pafupifupi makumi asanu kuyambira mchaka cha 1990 .
Bungweli lati zaka makumi awiri ndi zisanu zapitazo ana osapitirira zaka zisanu okwana 12.7 million anamwalira.
Malipoti a wayilesi ya BBC ati chaka chino chiwerengerochi kwa nthawi yoyamba chatsika ndi 6 miliyoni zomwe ikuyimilira ndi ma perecenti 53.
Kafukufukuyi wasonyeza kuti ana 16 000 osapitirira zaka zisanu akumamwalira tsiku ndi tsiku kamba ka matenda a chibayo,kutsekula mmimba ndi malungo ndipo kuti theka la imfazo limadza kamba kosowa zakudya zoyenera mthupi.