Mtsogoleri wampingo wakatolika wopuma Papa Benedict wa 16 ati ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe anthu othawa kwawo chifukwa cha nkhondo komanso anthu omwe amachoka m`mayiko mwawo kamba kosowa ntchito, akukumana nawo.
Mlembi wa Papa Benedict Arch bishop George Ganswein ndiye wanena izi atakhala nawo pamwambo wansembe ya ukaristia munzinda wa Ancona m`dziko la ITALY.
Arch bishop-yu anati Papa wopumayu ndi wokhudzidwa kwambiri kamba koti anthu ambiri akumataya miyoyo yawo pa nyanja nthawi yomwe akuwoloka kupita tsidya lina ndipo ati Papa Benedicto akuwapempherela.
Pamwambo wansembe ya ukaristiyayi , anapemphereranso anthu onse omwe akumakakamizika kuchoka m`mayiko mwawo kamba ka nkhondo komanso mavuto osiyanasiyana.