Chikondwelero cha mayimbidwe cha Radio Maria Malawi ati chikhala chopambana kusiyana ndi momwe zinthu zakhala zikuyendera mmbuyomu.
Wapampando wa komiti yoyendetsa chikondwelero cha mayimbidwe a Andrew Chiromo ndi omwe anena izi polankhulana ndi mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa za chikonzero cha mwambowu.
Iwo ati chikondwelerochi chisiyana ndi cha zaka zina kamba koti pali zinthu zatsopano zambiri.
Padakali pano makwaya omwe akuyembekezeka kutenga nawo mbali pa chikondwelerochi alipo okwana makumi atatu ochokera mma dayosizi a mdziko muno.