Mpingo wakatolika mdziko muno wati umazindikira kuti kukhala ndi mabanja abwino kungathandize chitukuko cha mpingo komanso dziko.
Episkopi wa dayosizi ya Chikwawa Ambuye Peter Musikuwa ndi omwe alankhula izi ku Limbe Cathedral mu Arkidayosizi ya Blantyre potsekera msonkhano waukulu wa bungwe la mabanja la Christian Family Movement CFM mdziko muno.
Ambuye Musikuwa ati mabanja abwino amapititsa mpingo patsogolo zomwe zimathandizanso chitukuko cha dziko.
Pamenepa iwo ati ndi udindo wa mabanja omwe achita nawo msonkhanowu kuthandiza mabanja anzawo pofuna kukhala ndi mabanja odalilika.
Polankhulapo mkulu wa bungweli m’chigawo cha kuno ku Africa banja la a Andrew ndi a Bernadetta Simango ati mabanja achita chotheka pogwiritsa ntchito mfundo zomwe aphunzira pa msonkhanowu.
Iwo ati ku msonkhanowu akambirananso mfundo za momwe angapititsire patsogolo bungweli kuti azipindula nawo.
Ku msonkhanowu kunafika akuluakulu a bungweli kuchokera mdziko la Mexico ndi cholinga chofuna kuzamitsa maziko a bungweli kuno ku Africa.