Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bambo Nsope Apempha Ophunzira a Sukulu ya Ukachenjede ya Chancellor Kukhala Opemphera

$
0
0

Ophunzira achikatolika ku Chancellor College mu mzinda wa Zomba awapempha kuti azikonda kulimbikitsa makhalidwe abwino ndi okonda kupemphera nthawi zonse.

 

Bambo Alfred Nsope ndi amene apereka pempholi pa m’bindikiro wa tsiku limodzi umene unachitikira ku sukuluyi.

 

Iwo ati kulimbikitsa moyo wa mapemphero kumathandiza kuti munthu azikhala odzadzidwa ndi mzimu woyera nthawi zonse.

 

Polankhulapo wapampando wa ophunzira achikatolika pa sukuluyi Charles Makalani ayamikira bambo Nsope kamba kowathandiza kudziwa njira zosiyanasiyana zomwe zimathandiza munthu kukhala ozama pachikhristu chake.

 

Iye wati potsatira zomwe aphunzira pa m’bindikirowo ziwathandiza kuti akhale ophunzira osinthika , ndipo zochita zawo zikhala zokhazo zomwe ndi zokomera mulungu nthawi zonse.

 

Mutu wa mbindikirowu unali “ntchito za mzimu woyera ndi mphatso zake


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>