Apolisi mdziko la Egypt apha mwa ngozi anthu khumi ndi awiri kuphatikizapo nzika ya mdziko la Mexico yomwe imakayenda mdzikolo.
Anthuwo amayenda mugalimoto zinayi zomwe zinalowa kumalo ena otetezedwa.
Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu okwana khumi ochokera mdziko la Mexico ndi la Egypt anavulazidwanso ndipo akulandira thandizo ku chipatala cha boma mdzikolo.
Mtsogoleri wa dziko la Mexico a Enrique Pena Nietowati ndi okhudzidwa ndi nkhaniyi ndipo wati akufuna kuti pakhale kafukufuku wamphamvu ndi boma la Egypt.