Apolisi m’boma la Ntchisi amanga mnyamata wina wa zaka 17 zakubadwa yemwe akumuganizira kuti waba njinga ya moto ya ndalama zosachepera 295 sauzande kwacha.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.
Iwo ati mnyamatayo Eniwelo Kagomba anaba njinga ya a Kayala Mthunzi loweruka lapitali pa nsika waukulu wa bomalo pa malo ena pomwe njingayo inayimikidwa pomwe iye amamwa mowa mgalimoto la nzake lomwe linayima pafupi ndi pomwe anayimitsa njingayo.
Kagomba atafika pamalowo ati amaona kuti a Mthunzi atalikira ndipo ati anaganiza zakuba njingayo.
A Mthunzi atayamba kuyang’ana anamuwona mnyamatayo akukoka njingayo ndipo pa nthawiyo apolisi amayenda mu nseumo.
A Mthunzi anafuula kupempha chithandizo ndipo apolisiwo anagwira mnyamatayo.
Mnyamatayo akuyembekezeka kukawonekera kubwalo lamilandu komwe akayankhe mulandu wakuba njinga.
A Kayala Mthunzi amachokera mmudzi wa Kapichira kwa mfumu yaikulu Malenga ndipo a Kagomba amachokera mmudzi mwa a Malenga kwa mfumu yayikulu Malenga m’boma lomwelo la Ntchisi.