Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

NDUNA IYAMIKIRA MGWIRIZANO PAKATI PA MIPINGO YA MU MZINDA WA MZUZU

$
0
0

 

Nduna ya za malimidwe ndi kuonetsetsa kuti m'dziko muno muli chakudya chokwanira Wolemekezeka a Peter Mwanza ayamikira mgwilizano wabwino omwe ulipo pakati pa Mipingo yozungulira  mzinda wa Mzuzu.

A Peter Mwanza omweso ndi phungu wa kunyumba ya malamulo wa dera la Mzuzu city wayamikira Mpingo wa Katolika, Lutheran komanso Anglican kaamba kochita mapemphero a njira ya mtanda limodzi.

 Akhristu a Mipingoyi anachitira limodzi mapempherowo pa 29 March 2013 lomwe ndi lachisanu loyera.

A Mwanza apemphanso akhristuwo  kuti apitilize kugwilizana monga momwe mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika Papa Francis akufunira kuti Mipingo izikhala pamodzi ndikumakambilana mfundo zothandiza kubweretsa mgwirizano pakati pawo.

 Akhristuwo anayenda kuchokera ku Moyale Barracks mpaka kufika ku tchalitchi cha Lutheran omwe ndi mtunda wa pafupifupi makilomita anayi.

Pakadali pano akhritu ambiri pa dziko lonse lapansi akukondwelera kuwuka kwa Ambuye Yesu Khristu.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>