Bambo Steven Saulosi Mkata omwe amwalira pa 30 March 2013 akuyembekezeka kuikidwa m’manda mwa ulemu lachiwiri likudzali pa 2 April 2013.
Monsignor Mkata adamwalira ku pachipatala cha St Joseph ku Nguludi m’boma la Chiradzulu atadwala kwa nthawi yaitali.
Iwo anabadwa mchaka cha 1922 ndipo anadzozedwa unsembe pa 15 August 1956 ku parishi ya Neno komwenso amkachokera.
Panthawi ya unsembe wawo, Monsignor Saulosi Mkata adatumikira m’maudindo osiyanasiyana mu Mpingo wa Katolika kuphatikizapo pa unduna wa episkopi omwe mtsogoleri wakale wa Mpingo wa Katokalika pa dziko lonse papa Benedikito wachi 16 opuma anawapatsa mchaka cha 2009.
Iwo amwalira akutumikira ngati wansembe othandizira ku parishi ya Limbe Cathedral mu arkidayosiziyo.
Ambuye Tarcius Ziyaye akuyembekezeka kutsogolera mwambo wa nsembe ya misa idzayambe 10 koloko m'mawa.
Imfa ya monsignor Steven Saulosi Nkata yadza patapita tsiku limodzi pomwe Mpingo wa katolika m'dziko muno watayanso Sisita Rose Mkhuwala a chipani cha Virgo Maria ku Nguludi mu arkidayosizi yomweyo ya Blantyre.
Thupi la malemu Sisista Rose Mkhuwala aliyika m’manda lolemba likudzali ku Nguludi komweko.
MZIMU WA MONSIGNOR STEVEN SAULOSI KOMANSO SISISTA ROSE MKHUWALA UWUSE NDI
MTENDERE.