Mkulu wa bungwe la atolankhani omwe anapezeka ndi Kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi la Journalists living with HIV and AIDS a David Kamkwamba apempha boma kuti lithandize pa nkhani yopereka malipiro abwino kwa anthu ogwira ntchito m’zipatala m’dziko muno kuti asamachoke n’kumakagwira ntchito m’mayiko ena.
A Kamkwamba ati boma likuyenera kupeza zipangizo zokwanira m’zipatala kuti ntchito yolimbana ndi matenda a Edzi idziyenda bwino m’dziko muno.
“Dziko lino lili ndi zinthu zina zomwe mayiko ena alibe ndipo n’koyenera kuti boma lidzigwilitsa bwino zinthuzi pofuna kupititsa patsogolo umoyo wa anthu m’dziko muno”, atero a Kankwamba.