A polisi ku Mzuzu agwira ndi kutsekera m'chitolokosi mwamuna wina yemwe amasunga mfuti ziwiri za mtundu wa Green nala m’boma la Karonga .
Mneneri wa a Polisi ku Mzuzu Sergeant Morris Chapola wati mwamunayo ndi Bonface Nkhamba wochokera m’mudzi wa Musenga kwa Mfumu yaikulu Wansambo m’boma la Karonga.
“A Nkhamba anali m’chitolokosi cha a polisi kale kaamba koti anapalamulanso milandu ina. Anthu akufuna kwabwino ndi omwe anatsina khutu apolisi kuti mkuluyo amasunga mfuti kunyumba kwake ku Karonga” atero a Chapola.
Malinga ndi a Chapola a Nkhamba amasunga mfutizo padenga la maudzu la nyumba yawo .
A Bonface Nkhamba akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa ndi kukayankha mlandu wopezeka ndi mfuti popanda chilolezo.