Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Francisco Akacheza Mdziko la America M’mwezi wa September

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco watsimikiza za ulendo wake wokacheza mdziko la America m’mwezi wa September chaka chino.

Polankhula kwa atolankhani omwe anali nawo paulendo wobwelera ku Rome, atatha kuyendera mayiko aku Asia kwa masiku asanu ndi limodzi, Papa Francisco anawuza atolankhaniwo kuti paulendo waku America, sadzayima mdziko la Mexico monga anthu ena akufalitsira,kamba koti adzakhala ndi zochita zambiri mdziko la America.

Paulendowu, mtsogoleri wa mpingo wa Katolikayu adzayendera maofesi a bungwe la mgwirizano wa mayiko  a United Nations ku likulu lake ku New York komanso Washington.

Papa Francisco anatsimikiza kale kuti paulendo womwewu, adzakhala nawonso pa msonkhano wa mabanja womwe udzachitikire mu mzinda wa Philadelphia mdziko lomwelo la America.

Pakadali pano likulu la mpingowu silidatsimikize ntchito zina zomwe Papa Francisco adzagwire akadzafika mdzikolo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>