Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapereka uthenga wachipepeso kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi ya chivomerezi mmayiko a Afghanistan ndi Pakistan.
Mu uthenga womwe Papa watumiza kudzera kwa nthumwi yake mdziko la Pakistan wati iye ndi wokhudzidwa ndi imfa, kuvulala komanso kusowa kwa anthu zomwe zadza kamba ka ngoziyi.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati iye ali nawo limodzi anthu omwe akhudzidwa pa ngoziyi kudzera mmapemphero. Ngozi ya chivomereziyi inachitika lolemba ndipo inapha anthu pafupifupi 400.