Bungwe la United Nations lati likugwirizana ndi mfundo yomwe bungwe la African Union lakhazikitsa, lochita kafukufuku wa maufulu a anthu omwe akhala akuphwanyidwa mdziko la Burundi.
Bungweli ati ndi lokhudzidwa ndi kupitlira kwa zamtopola zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo kuyambira pomwe mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunziza analengeza kuti apikisana nawo kachitatu pa chisankho cha Pulezidenti chomwe chinachitika mdzikolo.
Malipoti a nyuzi 24 ati bungweli lalonjeza kuti lichitapo kanthu pa zipolowe zomwe zikuchitika mdzikolo.
Bungweli lalonjezanso kuti liletsa mayendedwe a anthu komanso kutseka zitupa za anthu onse omwe akuthandizira pa zamtopolazi.
Anthu pafupifupi 200 anaphedwa ndipo ena 200 sauzande anathawa mdzikolo kamba ka mchitidwewu.