Chiwerengero cha achinyamata omwe amalandira mankhwala otalikitsa moyo a ARV ati chikukwera m’boma la Mangochi.
Mkulu oyang’anira anthu omwe amamwa mankhwalawa pa chipatala chachikulu cha Mangochi a Mike Nyirenda ndi omwe anena izi pa msonkhano womwe bungwe la Malawi Interfaith linakonzera akuluakulu a mipingo yosiyanasiyana m’boma la Mangochi ndi cholinga choti adziwe momwe ntchito yogawira mankhwala otalikitsa moyo kwa achinyamata ikuyendera m’bomali.
Iwo ati chiwerengero cha achinyamata olandira makhwalawa pa chipatalachi chikupitilira kukwera chikhazikitsireni zipatala za Teen Clinic zomwe zimatsekulidwa kamodzi pa mwezi ndi cholinga chofuna kupereka mpata kwa achinyamatawa kuti azifotokoza mavuto omwe akukumana nawo pa nthawi yomwe akumwa mankhwalawa.
Pamenepa iwo ati achinyamatawa akumakumananso ndi mavuto osiyanasiyana monga kusowa uphungu pa makhwala otalikitsa moyowa komanso kusalidwa ndi anthu omwe amawayang’anira ndipo apempha atsogoleri a mipingowa kuti akhale patsogolo pothetsa mchitidwe wosalana.
A Nyirenda anatinso ndi okhudzidwa kamba kakuchepa kwa chiwerengero cha abambo omwe amakayezetsa magazi ndipo anayamikira amayi a m’bomali kaamba koti nthawi zonse amakhala patsogolo kukayezetsa magazi kuti adziwe momwe mthupi mwao mulili.