Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

CHIPANI CHA AFORD CHAKANA KUGWIRA NTCHITO CHIPANI CHOLAMULA

$
0
0

 

Mmodzi wa akuluakulu a chipani cha Alliance For Democracy (AFORD) watsutsa zomwe  wayankhula wapampando wachipanichi  a Enock Chakufwa Chihana kuti chipani cha AFORD  chigwira ntchito ndi cha  People’s Party (PP) ponena kuti n’zamutu mwawo   osati maganizo a chipanichi.

A Chihana anauza mtundu wa a Malawi kuti chipani chawo chigwira ntchito ndi  cha People’s pa 20 April 2013 pa msonkhano wa chipani cha PP omwe unachitikira pa bwalo la zamasewelo la Lumbira ku Chilomoni mu mzinda wa Blantyre.

Pamsonkhanowo A Chihana anati sakuona mtsogoleri aliyense kumbali yotsutsa boma yemwe angachite zinthu ngati  mtsogoleri wa dziko lino Dr Joice Banda.

 A Msowoya ati izi zikungowonetsa kuti a Chihana siwoyenera kukhala mtsogoleri wachipanichi chifukwa  iwo sali ndi chidwi ndi chipani chawo cha AFORD.

“A Chihana akungofuna mpando wa unduna osati kuchita zinthu zokomera chipani cha AFORD  n’chifukwa chake abwera poyera kuti akusapota chipani cha Peoples”,atero a Msoyoya.

 

 

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>