Bwalo loyamba la milandu m’boma la Ntchisi lagamula sing’anga wina wa zaka 27 zakubadwa kuti akakhale ku ndende kwa zaka khumi ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kamba kopezeka olakwa pa mulandu wogwilira mayi wa zaka 35 zakubadwa.
Wapolisi wofalitsa nkhani m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.
Iwo ati Sing’angayo yemwe amadziwika ndi dzina loti Willard Jabesi Njovu anapalamula mlanduwu pa 16 mmwezi wa September, pomwe mayiyo Emlida Mwale anapita kwa sing’angayo kukafuna thandizo la mankhwala kamba kosowa mphatso ya mwana m’banja mwawo.
“Mayiyu atapita kwa singangayo anamuwuza kuti avule zovala kuphatikizapo chovala cha mkati, ndipo anamuza kuti agone ndi cholinga choti amuwunike, pambuyo pake ndi pomwe anamugwililira,”anatero Sergent M’bumpha.
Iwo anapitiliza ponena kuti singangayo anauza mayiyu kuti asakanene kwa anthu kamba alodzedwa koma mayiyu atabwelera kumudzi anakauza mwamuna wake yemwe anakanena nkhaniyi ku polisi.
A Willard Jabesi Njovu amachokera m’mudzi mwa Mingu kwa mfumu yaikulu Choolo m’boma la Ntchisi.