Ark Episkopi wa Arch Dayosizi ya Lilongwe Ambuye Tarsizius Ziyaye apempha akhristu a m’parishi ya St Kizito mu Ark dayosiziyo kuti alimbikitse m’gwirizano wabwino pakati pawo.
Ambuye Ziyaye anena izi lamulungu pa mwambo wokhazikitsa bukhu la ndondomeko za chitukuko m’parishiyi.
Iwo ati mapulani a zachitukuko omwe parishiyo yakonza ndi osavuta kuwakwaniritsa pokhapokha atamanga mgwirizano pakati pawo