Bungwe lowona ma ufulu a anthu mchipembedzo cha Chisilamu la Muslim Forum for Democracy lalangiza mabungwe omenyera ufulu wa anthu mdziko muno,kuti athandize anthu omwe akhudzidwa ndi mvula ya mphamvu yomwe yakhala ikugwa mdziko muno.
Wapampando wa bungweli Sheikh Jafar Kawinga ndi yemwe wapereka langizoli ,pomwe bungweli mogwirizana ndi bungwe la Al-barakah Charity Trust, limapereka katundu wosiyanasiyana kwa anthu omwe akhudzidwa ndi mvula yamphamvu mdera la group Mkupu mfumu yayikulu Kadewere mboma la Chiradzuru..
Sheikh Kawinga wati mabungwe omenyera ufulu wa anthu , padakali pano angokhala chete pomwe anthu omwe amati amawayimilira, akuvutika ndi vuto la kusefukira kwa madzi. Pamenepa iwo ati nthawi yakwana yoti mabungwewa awonetse mbali yawo pothandiza anthuwa pomwe ali pamavuto osiyanasiyana kamba ka mvulayi.