Bungwe lowona za ufulu wa anthu padziko lonse la Amnesty International,lati dziko la Nigeria lalephera kuteteza mzika zake zomwe zikukhala mdera la Baga,pamene gulu la zigawenga la Boko Haram lawopseza kuti lichita zamtopola mderalo.
Malipoti ena ati akusonyeza kuti anthu pafupifupi zikwi ziwiri aphedwa mderalo mmwezi wa December okha chaka chatha,koma boma la Nigeria likungotchula chiwelengero cha anthu 150 okha kuti ndi omwe aphedwa mmweziwo paziwembu zomwe zigawengazo zakhala zikuchita mderalo.
Padakali pano, mmodzi mwa akuluakulu a asilikali mdzikolo yemwe sadafune kutchulidwa dzina,ati wawuza bungweli kuti ngakhale boma silikuchitapo kanthu,gululo lawopseza zochita chiwembu mdera la Baga.
Pothilirapo ndemanga mneneri wa asilikali a boma mdzikolo wauza mtolankhani wa BBC kuti asilikali ali okonzeka mderalo pomwenso akumayendera matauni ake pafupipafupi