Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika Ambuye Montfort Sitima wapempha makwaya mdziko muno kuti aziwonetsetsa nthawi zonse kuti pamene akupeka nyimbo zizikhala za tanthauzo.
Ambuye Sitima amalankhula izi lamulungu ngati mlendo wolemekezeka pomwe kwaya ya St Patricks yochokera ku parish ya St Augustine Cathedral mu dayosiziyi imakhazitsa chimbale cha nyimbo zowonera.
Iwo ati makwaya akamapeka nyimbo zawo aziwonetsetsa kuti zikugwirizana ndi chiphunzitso cha mpingo wakatolika.
Pamenepa Ambuye Sitima ayamikira kwayayi pa luso lomwe ili nalo lofalitsa uthenga wabwino kudzera mmayimbidwe.