Mpingo wa katolika ku Vatican wakhazikitsa malo ometera awulele a anthu osowa kwawo.
Pa mwambowu womwe unatsekuliridwa ndi mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco kunafika anthu ochuluka osowa kwawo kudzametetsa.
Anthu odzipereka ndi amene azigwira ntchito yometa anthuwa tsiku lolemba lililonse kamba koti pa tsikuli malo onse ometera mdzikolo amakhala otseka.
Izi zadza pambuyo pokhazikitsa malo omwe anthuwa azitha kukasambako omwe azikhala otsekula tsiku lililonse kupatula tsiku lachitatu lomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu amakhala akusonkhana ndi akhristu kudzanso alendo osiyanasiyana omwe amafika ku likulu la mpingowu.