Mtsogoleri wa gulu la zigawenga za Boko Haram Abubakar Shekau, wanenetsa kuti alepheretsa zisankho za atsogoleri zomwe dzikolo likuyembekezeka kukhala nazo pa 28 March chaka chino.
Iye wanena izi kudzera pakanema wina yemwe gululo latulutsa pambuyo pachiwembu chomwe gulolo lachita mdera lakumpoto chakumvuma kwa dzikolo.
Anthu 38 afa pachiwembucho.
Iye wanenetsa kuti chisankhocho, sichichitika ngakhale iye atamwalira lisanafike tsiku la zisankholo.
Boma la Nigeria lidavomereza kale kuti ntchito yovota, itha kudzakhaladi yovutirapo maka mdera la ku mpoto chamvuma komwe gululo lapha anthuwo posachedwapa.