Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati pofuna kulowa pa khomo la nyumba ya atate akhristu akuyenera kuzindikira za chifundo chomwe Mulungu ali nacho pakati pa wina aliyense.
Papa analankhula izi lachiwiri ku likulu la mpingowu pomwe amatsekulira chaka cha chifundo cha Mulungu.
Iye wati pa nthawiyi mpingo komanso akhristu akuyenera kuchita ntchito zachifundo komanso akhale okhululuka.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati chakachi chithandiza akhristu kulapa machimo awo komanso kuwazindikiritsa kuti Mulungu ndi wachifundo kaamba koti amakhululuka.
Pa mwambowu Papa anatsekula khomo loyera ku tchalitchi cha St Peter’s Basilica pofuna kutanthauza kuti aliyense wodzera khomo limenelo alandira chifundo cha Mulungu.
Mwambowu upitilira lamulungu pomwe Papa akatsekule khomo loyera la St John Lateran Cathedral komanso ma Episkopi onse a mpingowu pa dziko lonse akachitanso chimodzimodzi mma tchalitchi awo.
Dayosizi ya mpingo wakatolika ya Mangochi lachiwiri unagwilizana ndi mpingowu pa dziko lonse kuchita mwambo wotsekulira chaka cha chifundo cha mulungu.
Mwambo wa nsembe ya misa yotsekulira chakachi mu dayosiziyi unachitikira ku St Augustine Cathedral ndipo Episkopi wa dayosiziyi ambuye Montfort Sitima ndi omwe anatsogolera mwambowu.
Iwo ati kudzera mu chakachi Mulungu akuyitana kuti tikhale ndi mtima wokhululuka kuti chifundo chake chiwonekere pakati pa wina aliyense.
Iwo ati mu chakachi akhristu akuyenera kulimbikitsa ntchito za chifundo ndi zina.