Mabungwe omenyala ufulu wa anthu mdziko la Egypt apempha boma la dzikolo kuti likhwimitse chitetezo ku mipingo ya mdzikolo.
Ma bungwewa apereka pempheloli potsatira chiwopsezo chomwe mpingo wa Orthodox walandira kuchokera ku gulu la zauchifwamba la Jihadist.
Gululi ati likukonza zokachita zamtopola pa tchalitchi lina la mpingowu ndipo popereka chiwopsezocho lachita kufotokoza malo omwe tchalitchilo limapezeka komanso mmene chinamangidwira.
Padakali pano apolisi mdzikolo ati ayamba kale kuteteza malowo.
Gulu la Jihadist lakhala likupereka chiwopsezo ku magulu osiyanasiyana mdzikolo ndipo mu chaka cha 2011 gululi linachita zamtopola pa tchalitchi lina mdzikolo pomwe anthu okwana 26 anaphedwa.