Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ndiwokhudzidwa ndi kuchuluka kwa anthu omwe amachita malonda ogulitsa mankhwala ozunguza bongo.
Papa Francisco amalankhula izi poyankha mafunso a atolankhani a nyumba ina yotsindikiza nkhani yomwe achinyamata a mdziko la kwawo ku Argentina akhazikitsa posachedwapa.
Atolankhaniwo amafuna kumva mayankho a Papa pankhani zosiyanasiyana, zomwe ndi kuphatikizapo mavuto omwe akudza chifukwa cha kuchuluka kwa anthu omwe akuchita malondawa.
Iye wati akukonza dongosolo lokacheza mdziko la Argentina mchaka cha 2016 pofuna kuti athe kudziwonera yekha momwe zinthu zikuyendera pankhaniyi mdzikolo ndinso mmayiko ena omwe akukhudzidwa ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo a malonda ogulitsa mankhwalawa.