Mpingo wa katolika ku Vatican wabwereza kupempha mayiko pa dziko lonse kuti athetse lamulo la kupha kwa anthu olakwira malamulo.
Kazembe wa mpingowu ku bungwe la m’gwirizano wa maiko la United Nations Arch-bishopu Silvano Thomas ndi yemwe wapereka pempholi pa msonkhano wa nthambi yowona za ufulu wa anthu ku bungwe la Human Rights Council.
Iye wauza nthumwi ku msonkhanowo kuti mpingo wa katolika umakhulupilira kulemekeza moyo choncho mpofunika kuti mayiko achotse lamuloli poika zilango zina.
Ambuye Thomas ati ngakhale kupha kumawoneka ngati njira yokhayo yomwe ingachepetse milandu yakupha, koma kusintha kwenikweni sikukuwoneka.