Bwalo lalikulu lamindu mdziko la South Africa lagamula kuti mtsogoleri wa dzikolo a Jacob Zuma anaphwanya lamulo polephera kubweza ndalama za boma zomwe anagwiritsa ntchito pochitira chitukuko dera la kwao.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC bwalolo lapereka masiku makumi asanu ndi limodzi ku nthambi yoona za chuma mdzikolo kuti yiwokhetse ndalama zomwe Pulezident Zuma akuyenera kubweza.
Chigamulocho ati chabweretsa chimwemwe kwa zipani zotsutsa boma mdzikolo zomwe ati ziyesetsa kuti Pulezidenti Zuma atule pansi udindowu.
Malipoti ati akuluakulu a chipani cholamula cha African National Congress ANC akhala pansi kuti akambirane za chigamulochi.
Ngakhale pulezidentiyu wagamulidwa, iye akutsutsabe kuti palibe chomwe analakwitsa.