Ark-episkopi wa mzinda wa Vienna mdziko la Australia Ambuye Christopher Schonborn wati chifundo cha Mulungu chilipo kwa aliyense amene amakhala akusawutsidwa mu mtima.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Ambuye Schonborn amalankhula izi dzulo potsekulira msonkhano wa chifundo cha Mulungu wa masiku anayi wa ma episkopi a ku Europe omwe ukuchitikira mu mzinda wa Rome mdziko la Italy.
Iwo anawunikira kusiyana komwe kulipo pakati pa umunthu ndi chifundo cha Mulungu potengera kuti anthu ambiri amawonetsa chifundo chabodza akafuna kuthana ndi vuto lomwe akukumana nalo.
Mwa zina ku msonkhanowu ma episkopi-wa ndi mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco mawa akuyembekezeka kuchita mapemphero opemphelera onse omwe akudzipereka pochitira chifundo ena pa bwalo la St Peters komanso pa tsiku laMulungu lomwe ndi la chifundo chaMulungu akachita nawo mwambo wa nsembe ya misa.