Apolisi m’boma la Ntchisi akusunga mchitokosi amuna atatu kamba kowaganizira kuti amalima chamba.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.
Sergent M’bumpha wati amunawa a Davis Mzunga a zaka 38 a mmudzi mwa Chikowa, a Austin Kambewa a zaka 37 a mmudzi mwa Kawenje ndi a Petro Kadammanja a zaka 40 a mmudzi mwa Kachirandozi onsewa a kwa mfumu yaikulu Chilooko m’bomalo amalima chambachi mmidzi yomwe amakhalayi.
Malinga ndi malipoti, polisi yaying’ono ya Malomo ndi yomwe inalandira uthenga wa mchitidwewu kuchokera kwa mafumu a mmidziyi, ndipo apolisiwa motsogozedwa ndi Sub Inspector Orphan Mkhalipi anapita kukazula chambacho chomwe chinali chitayamba kukhwima.
Amunawo ati avomera za mchitidwewu ndipo akawonekera ku bwalo lamilandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wolima chamba.