Apolisi m`dziko la South Africa ati anayimitsa galimoto la mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha Economic Freedom Fighters (EFF) a Jullious Malema, potsatira zomwe mkuluyu ananena masiku apitawa kuti mtsogoleri wa dzikolo a Jacob Zuma atule pansi udindo wawo.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, a Zuma akuwadzudzula kuti anasakaza ndalama za boma pokozetsera nyumba yawo yapadera.
Chipani va EFF chati apolisi anayimitsa galimoto ya mkuluyu munzinda wa Johannesburg ndi kumulozetsa mfuti ngati njira imodzi yomuopseza.
A Zuma ati akukana kuti anawononga ndalamazi koma avomera kuti abweza.