Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati akhristu a mpingo wakatolika ndi Methodists akuyenera kuphunzirana kamba koti zolinga zawo ndi zimodzi.
Papa Francisco amalankhula izi pomwe akuluakulu a mpingo wa Methodists a ku Europe ndi Britain amatsekulira ofesi yawo mu mzinda wa Rome.
Papa wati ngakhale akhristu a mipingoyi saganiza mofanana potengera ziphunzitso zake, akuyenera kugwilira ntchito limodzi kamba koti cholinga chawo ndi chimodzi.
Iye wati pomwe mpingowu wakhazikitsa ofesi mu mzindawu, zithandiza kuti umodzi wa mipingoyi upite patsogolo komanso kukonza zovuta zomwe zinalipo pakati pawo.