Dziko la Egypt lati litumiza zomwe lapeza pa kafukufuku wokhudza kuphedwa kwa ophunzira wa mdziko la Italy yemwe anapezeka atafa m`dziko la Egypt.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, ophunzirayo Giulio Regen wa zaka 28 yemwe amachita kafukufuku wa maphunziro ake mdziko la Egypt anapezeka atafa mphepete mwa msewu wina.
Apolisi a dziko la Egypt akuyembekezeka kupereka kafukufuku wa nkhaniyi ku dziko la Italy lomwe ati silikukhutira ndi momwe dziko la Egypt likuchitira kafukufukuyu.
Anthu m`dziko la Italy amaganiza kuti ophunzirayu anachitidwa chiwembu ndi nthambi ya boma ya ukazitape ya dziko la Egypt kamba ka kafukufuku wokhudza anthu ogwira ntchito komanso kumenyera maufulu a anthu ndipo dziko la Egypt likukana za nkhaniyi.