Bungwe la ma Episkopi a mpingo wa Katolika m’dziko la Burundi lati silikugwirizana ndi zomwe m’tsogogoleri wa dzikolo akufuna kuti adzayimenso pa chisankho cha president kamba koti matelemu ake okhalira paudindowu anatha.
M’tsogoleri wa dziko la Burundu-yu a Piere Nukurunziza akuti akufunanso kudzapikisana nawo kachitatu, pachisankho zomwe ndi zotsutsana ndi malamulo a dzikolo amene amapereka mwayi kwa president kulamulira dzikolo kwa ma telemu ake awiri , kenaka atule pansi udindo wake.
Pamenepa bungwe la ma episkopiwa lapereka kalata ku boma yotsutsa maganizo a m’tsogoleriyu.
Malingana ndi malipoti a Catholic World News bungwe la ma Episkopi a mpingo wa Katolika ndi limodzi mwa mabungwe amipingo amene amadzipereka pomenyera ufulu wa anthu m’dziko la Burundi.