Akuluakulu oyendetsa ntchito za Radio Maria pa dziko lonse alengeza zakubadwa kwa wailesi ina m’dziko la Madagascar
Kukhadzikitsidwa kwa wailesiyi kwachulukitsa nambala ya mayiko amene ali ndi Radio Maria m’mayiko a mu Africa ndipo yafika pa 19 tsopano.
Wailesiyi iyamba kuwulutsa mawu ndi mapulogalamu ake kuyambira pa 25 April , ndipo likulu lake alikhadzikitsa mu diocese ya mpingowu ya Ambositra yomwenso ili ndi akhristu ambiri a mpingo wa Katolika.
Wayilesiyi inayamba kuwulutsa mawu pa 25 March chaka chino, ndipo idzakhazikitsidwa pa 28 April chaka chomwechino. Mwa zina wailesiyi iziwulutsa ma pologalamu othandiza anthu kumvetsa bwino za chiphunzitso cha mpingo wa Katolika, kulimbikitsa mapemphero, umodzi , chisamaliro cha anthu ndi ena ambiri monga momwe wailesizi zimachitira padziko lonse .
Polankhula m’modzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito za wailesizi m’mayiko a mu Africa , Bambo Jean Paul Kayihura ayamikira mayiko ndi ena onse amene anatengapo mbali pothandiza ndi ndalama zokhadzikitsira wailesiyi.
Dziko la Malawi kudzera ku Radio Maria ndi limodzi mwa mayiko amene anachitapo kanthu potolera ndalama zothandizira pa ntchito yokhadzikitsa wailesiyi kudzera pa Mariatona amene anachika m’chaka cha 2014.
Bambo Kayihura ati wailesi ina ikuyembekezeka kukhadzikitsidwanso m’dziko la Guinea Conakry posachedwapa.