Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti amuyikize mmapemphero pomwe akukonzekera ulendo wake wokayendera anthu othawa kwao pa doko la Lesbos mdziko la Greece loweruka likudzali.
Papa wapereka pempholi ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mkumano omwe amakhala nawo lachitatu lililonse ndi anthu osiyanasiyana.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican pa ulendowu omwe Papa wachita kuyitanidwa ndi mtsogoleri wa mpingo wa Orthodox Bartholomew I komanso mtsogoleri wa dziko la Greece, akuyembekezeka kupita ndi atsogoleri a mpingowu osiyanasiyana ndi cholinga chofuna kukawonetsa umodzi wake kwa anthuwo ngakhalenso mzika za dzikolo kaamba kowalandira anthuwa mwa chikondi.
Padakali pano dziko la Greece likusungira anthu othawa kwao pafupifupi 1 miliyoni ambiri mwa iwo omwe akuthawa nkhondo mdziko la Syria.