Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ambuye Musikuwa ati Achinyamata Akhale a Makhalidwe AbwinoAmbuye Musikuwa ati Achinyamata Akhale a M

$
0
0

Episkopi wa mpingo wakatolika wa dayosizi ya Chikwawa, Ambuye Peter Musikuwa walangiza ophunzira msukulu zosiyanasiyana za ukachenjede m’dziko muno kuti asalore kuti ena aziwapotoza ndi kuti azitsatira ziphunzitso zabodza zomwe zikumbikitsa makhalidwe oyipa pakati pawo.

Ambuye Musikuwa anena izi pambuyo pa msonkhano wa masiku atatu wa ophunzira a chikatolika msukulu za ukachenjede mdziko muno omwe unayamba pa 8 ndi kutha pa 10 m’boma la Salima.

Iwo ati kuti izi zitheke  mosavuta, ophunzirawa akuyenera kukhala ozama mu chikhulupiliro chawo.

“Achinyamatawa tawapempha kuti akhale osunga chikhulupiliro chawo cha katolika monga adachitira  apostoli komanso  owonetsa chitsanzo chabwino kwa anzawo,” anatero Ambuye Musikuwa.

Iwo ati achinyanata akuyenera  kusunga bwino zomwe adaphunzitsidwa za chikatolika komanso zikhulupiliro zimene Eklezia katolika amaphunzitsa.

Ambuye Musikuwa ati,  “achinyamata sakuyenera kukhala otsogolera pa zinthu zoyipa koma  nthawi zonse akhale nyale ndiponso mchere wokometsa makhalidwe, mayendedwe ndiponso ntchito za achinyamata anzawo.”

Polankhulanso m’modzi mwa ophunzira ku sukulu  ya Malawi University Science and Technology (MUST) Blessings Masina anayamikira mpingowu kamba kowakonzera dongosolo  labwino la msonkhanowu kamba koti atha kumvetsa bwino zambiri zochitika mu mpingowu.

Malingana ndi Bambo Vincent Mwakhwawaomwe ndi mkulu wa achinyamata ku likulu la mpingowu m’dziko muno mpingo wakatolika unakonza msonkhanowu kuti uthandize ophunzirawa kudziwa bwino zambiri zokhudza mpingowu.

“Tinakonza msonkhanowu kuti uthandize achinyamatawa kukhala nzika komanso atsogoleri abwino a mpingo,” anatero bambo Mwakhwawa.

Bambo Mwakhwawa ati anali okondwa momwe achinyamata anafikira ku msonkhanowu poganizira kuti zochita zimakhala zambiri kusukulu.

Achinyamata achikatolika omwe anasonkhana ku msonkhanowu anali ochokera msukulu zonse za ukachenjede za mdziko muno.

Trending Articles

Mdima unadetsa dziko

<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>